Kodi ndizotheka kuti munthu kapena mpingo wotchedwa wa Mulungu kumachita ntchito za chifundo ngati kugawa chimanga koma uli wabodza? A Kennedy Gondwe ochokera ku Centers for Apologetics Research (CFAR) akuti ndizotheka. Iwo akulongosora kuti ntchito za chifundo sizokwanira kumupangitsa munthu kapena mpingo kukhala owona. Iwo akuyamba kutiwuza maonekedwe eneeni a mipingo yabodza awiri.
